Ndipo Sarai anati kwa Abramu, kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m'maso mwake: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine.
1 Samueli 20:23 - Buku Lopatulika Ndipo za chija tinakambirana iwe ndi ine, taona, Yehova ali pakati pa ife nthawi zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo za chija tinakambirana iwe ndi ine, taona, Yehova ali pakati pa ife nthawi zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono pa zimene tapanganazi, Chauta ndiye mboni pakati pa ine ndi iwe mpaka muyaya.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono zimene tapanganazi Yehova ndiye mboni pakati pa iwe ndi ine mpaka muyaya.” |
Ndipo Sarai anati kwa Abramu, kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m'maso mwake: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine.
ndi Mizipa, chifukwa kuti anati, Yehova ayang'anire pakati pa ine ndi iwe, pamene tisiyana wina ndi mnzake.
Ukasautsa ana anga aakazi, kapena ukatenga akazi kuonjezera pa ana anga, palibe munthu mmodzi ali nafe; taonani, Mulungu ndiye mboni yanga ndi yako.
Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu wa Nahori, Mulungu wa atate wao aweruze pa ife. Ndipo Yakobo analumbirira pa Kuopsa kwa atate wake Isaki.
Chomwecho Davide anabisala kuthengo; ndipo pakukhala mwezi, mfumu inakhala pansi kudya.
Ndipo Yonatani ananena kwa Davide, Muka mumtendere, popeza tonsefe tinalumbira m'dzina la Yehova, kuti, Yehova adzakhala pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa mbeu yako, nthawi zamuyaya. Ndipo iye ananyamuka nachoka; koma Yonatani anamuka kumzinda.