Ndipo taona, ndidzatumiza mnyamatayo, ndi kuti, Kafune miviyo. Ndikamuuza mwanayo, kuti, Taona mivi ili chakuno; uitole nubwere, popeza pali mtendere kwa iwe, palibe kanthu, pali Yehova.
1 Samueli 20:22 - Buku Lopatulika Koma ndikati kwa mnyamatayo, Ona mivi ili kutsogoloko; pamenepo unyamuke ulendo wako; popeza Yehova wakuuza umuke. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ndikati kwa mnyamatayo, Ona mivi ili kutsogoloko; pamenepo unyamuke ulendo wako; popeza Yehova wakuuza umuke. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ndikamuuza mnyamatayo kuti, ‘Mivi ili patsogolo pako,’ pomwepo iweyo uchoke, pakuti Chauta ndiye wati uchokepo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ndikadzati, ‘Taona mivi ili patsogolo pako,’ iwe udzachoke chifukwa Yehova ndiye walola kuti uchokepo. |
Ndipo taona, ndidzatumiza mnyamatayo, ndi kuti, Kafune miviyo. Ndikamuuza mwanayo, kuti, Taona mivi ili chakuno; uitole nubwere, popeza pali mtendere kwa iwe, palibe kanthu, pali Yehova.
Ndipo mnyamatayo atafika pamalo a muvi umene Yonatani anauponya, Yonatani anafuulira mnyamatayo, nati, Muviwo suli m'tsogolo mwako kodi?
Ndipo Yonatani ananena kwa Davide, Muka mumtendere, popeza tonsefe tinalumbira m'dzina la Yehova, kuti, Yehova adzakhala pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa mbeu yako, nthawi zamuyaya. Ndipo iye ananyamuka nachoka; koma Yonatani anamuka kumzinda.