Ndipo padzakhala kuti, ngati iwo adzaphunzira mwakhama njira za anthu anga, kulumbira ndi dzina langa, Pali Yehova; monga anaphunzitsa anthu anga kulumbira pali Baala; pamenepo ndidzamangitsa mudzi wao pakati pa anthu anga.
1 Samueli 20:21 - Buku Lopatulika Ndipo taona, ndidzatumiza mnyamatayo, ndi kuti, Kafune miviyo. Ndikamuuza mwanayo, kuti, Taona mivi ili chakuno; uitole nubwere, popeza pali mtendere kwa iwe, palibe kanthu, pali Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo taona, ndidzatumiza mnyamatayo, ndi kuti, Kafune miviyo. Ndikamuuza mwanayo, kuti, Taona mivi ili chakuno; uitole nubwere, popeza pali mtendere kwa iwe, palibe kanthu, pali Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ndidzatuma mnyamata wanga kuti akatole miviyo. Mnyamatayo ndikamuuza kuti, ‘Mivi ili chakuno, kaitole!’ Pomwepo iweyo udzatuluke, chifukwa ndikulumbira, pali Chauta wamoyo, kuti kuli mtendere, iwe sudzakhala pa zoopsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ndidzatuma mnyamata ndi kuti, ‘Pita ukatole miviyo!’ Ngati ndidzanena kwa iye kuti, ‘Taona, mivi ili mbali yakuno, kayitole,’ iwe ukatuluke, pakuti ndikulumbira, pali Yehova Wamoyo, ndiye kuti zako zili bwino, palibe choopsa chilichonse. |
Ndipo padzakhala kuti, ngati iwo adzaphunzira mwakhama njira za anthu anga, kulumbira ndi dzina langa, Pali Yehova; monga anaphunzitsa anthu anga kulumbira pali Baala; pamenepo ndidzamangitsa mudzi wao pakati pa anthu anga.
Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.
Iwo akulumbira ndi kutchula tchimo la Samariya, ndi kuti, Pali Mulungu wako, Dani; ndipo, Pali moyo wa njira ya ku Beereseba, iwowa adzagwa, osaukanso konse.
Koma ndikati kwa mnyamatayo, Ona mivi ili kutsogoloko; pamenepo unyamuke ulendo wako; popeza Yehova wakuuza umuke.
Ndipo anauza mnyamata wakeyo, Thamanga uzikatola mivi imene ndidzaponya; ndipo analikuthamanga mnyamatayu, iye anaponya muvi kuutumphitsa iye.