Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe, mbale wanga Yonatani; wandikomera kwambiri; chikondi chako, ndinadabwa nacho, chinaposa chikondi cha anthu aakazi.
1 Samueli 20:17 - Buku Lopatulika Ndipo Yonatani anamlumbiritsa Davide kachiwiri, chifukwa anamkonda; popeza anamkonda monga anakonda moyo wa iye yekha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yonatani anamlumbiritsa Davide kachiwiri, chifukwa anamkonda; popeza anamkonda monga anakonda moyo wa iye yekha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Yonatani adalumbiritsanso Davide kuti asaleke kumkonda, pakuti Yonatani ankakonda Davide monga momwe ankadzikondera iye mwini. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yonatani anamulumbiritsanso Davide kuti asaleke kumukonda, pakuti ankamukonda monga ankadzikondera yekha. |
Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe, mbale wanga Yonatani; wandikomera kwambiri; chikondi chako, ndinadabwa nacho, chinaposa chikondi cha anthu aakazi.
Ndipo Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani anawalumbirira iwo ndi anthu ao, kuti, Musaope kuwatumikira Ababiloni; khalani m'dzikomu, mutumikire mfumu ya ku Babiloni, ndipo kudzakukomerani.
Mbale wanu, ndiye mwana wa mai wanu, kapena mwana wanu wamwamuna, kapena mwana wanu wamkazi, kapena mkazi wa kumtima kwanu, kapena bwenzi lanu, ndiye ngati moyo wanuwanu, akakukakamizani m'tseri, ndi kuti, Tipite titumikire milungu ina, imene simunaidziwe, inu, kapena makolo anu;
Ndipo kunali, pakutsiriza iye kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.
Pamenepo Yonatani ndi Davide anapangana pangano, pakuti adamkonda iye ngati moyo wa iye yekha.