Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 20:15 - Buku Lopatulika

komanso usaleke kuchitira chifundo a m'nyumba yanga nthawi zonse: mungakhale m'tsogolomo Yehova atathera adani onse a Davide padziko lapansi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

komanso usaleke kuchitira chifundo a m'nyumba yanga nthawi zonse: mungakhale m'tsogolomo Yehova atathera adani onse a Davide pa dziko lapansi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pamene Chauta adzaŵatha adani onse a Davide pa dziko lapansi,

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo usadzaleke kuchitira chifundo banja langa. Pamene Yehova adzawatha adani onse a Davide pa dziko lapansi.”

Onani mutuwo



1 Samueli 20:15
7 Mawu Ofanana  

Koma undikumbukire ine m'mene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipo undichitiretu ine kukoma mtima: nunditchule ine kwa Farao, nunditulutse ine m'nyumbamu:


Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, chifukwa cha lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Yonatani mwana wa Saulo.


Ndipo undionetsere chifundo cha Yehova, si pokhala ine ndi moyo pokha, kuti ndingafe;


Ndipo za chija tinakambirana iwe ndi ine, taona, Yehova ali pakati pa ife nthawi zonse.


Ndipo Yonatani ananena kwa Davide, Muka mumtendere, popeza tonsefe tinalumbira m'dzina la Yehova, kuti, Yehova adzakhala pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa mbeu yako, nthawi zamuyaya. Ndipo iye ananyamuka nachoka; koma Yonatani anamuka kumzinda.


Chifukwa chake tsono undilumbirire ndi Yehova, kuti sudzatha mbeu yanga nditamuka ine, ndi kuti sudzaononga dzina langa m'nyumba ya atate wanga.