Koma undikumbukire ine m'mene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipo undichitiretu ine kukoma mtima: nunditchule ine kwa Farao, nunditulutse ine m'nyumbamu:
1 Samueli 20:14 - Buku Lopatulika Ndipo undionetsere chifundo cha Yehova, si pokhala ine ndi moyo pokha, kuti ndingafe; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo undionetsere chifundo cha Yehova, si pokhala ine ndi moyo pokha, kuti ndingafe; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikakhala ndili moyobe, udzandiwonetse kukoma mtima konga kwa Chauta. Koma ndikafa, usadzaleke kuchitira chifundo banja langa mpaka muyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikakhalabe ndi moyo udzandionetse kukoma mtima monga kwa Yehova nthawi yonse ya moyo wanga, kuti ine ndisaphedwe. |
Koma undikumbukire ine m'mene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipo undichitiretu ine kukoma mtima: nunditchule ine kwa Farao, nunditulutse ine m'nyumbamu:
Ndipo Davide anati, Kodi atsalako wina wa nyumba ya Saulo, kuti ndimchitire chifundo chifukwa cha Yonatani?
Ndipo mfumu inati, Kodi atsalanso wina wa nyumba ya Saulo kuti ndimuonetsere chifundo cha Mulungu? Ziba nanena ndi mfumu, Aliponso mwana wa Yonatani wopunduka mapazi ake.
Mulungu alange Yonatani, ndi kuonjezapo, ngati atate wanga akondwera kukuchitira choipa, ine osakuululira, ndi kukuchotsa kuti upite mumtendere; ndipo Yehova akhale nawe, monga anakhala naye atate wanga.
komanso usaleke kuchitira chifundo a m'nyumba yanga nthawi zonse: mungakhale m'tsogolomo Yehova atathera adani onse a Davide padziko lapansi.
Ndipo za chija tinakambirana iwe ndi ine, taona, Yehova ali pakati pa ife nthawi zonse.
Chifukwa chake tsono undilumbirire ndi Yehova, kuti sudzatha mbeu yanga nditamuka ine, ndi kuti sudzaononga dzina langa m'nyumba ya atate wanga.