1 Samueli 20:10 - Buku Lopatulika Tsono Davide anati kwa Yonatani, Adzandiuza ndani ngati atate wako alankhulira iwe mokalipa? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsono Davide anati kwa Yonatani, Adzandiuza ndani ngati atate wako alankhulira iwe mokalipa? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Davide adafunsa Yonatani kuti, “Kodi ndani amene adzandiwuze, abambo ako akakuyankha mokalipa?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anafunsa kuti, “Adzandiwuza ndani ngati abambo ako akuyankhe mwaukali?” |
Ndipo Yosefe anaona abale ake, ndipo anazindikira iwo, koma anadziyesetsa kwa iwo ngati mlendo, nanena kwa iwo mwankhanza: ndipo anati kwa iwo, Mufuma kuti inu? Nati iwo, Ku dziko la Kanani kudzagula chakudya.
Ndipo Yonatani anati, Iai ndi pang'ono ponse; ine ndikadziwa konse kuti atate wanga anatsimikiza mtima kukuchitira choipa, sindidzadziwitsa iwe kodi?
Koma Nabala anayankha anyamata a Davide nati, Davide ndani? Ndi mwana wa Yese ndani? Masiku ano pali anyamata ambiri akungotaya ambuye ao.
Koma mnyamata wina anauza Abigaile, mkazi wa Nabala, kuti, Onani, Davide anatumiza mithenga akuchokera kuchipululu kulonjera mbuye wathu; koma iye anawakalipira.
Chifukwa chake tsono mudziwe ndi kulingalira chimene mudzachita; popeza anatsimikiza mtima kuchitira choipa mbuye wathu, ndi nyumba yake yonse; popeza iye ali woipa, ndipo munthu sakhoza kulankhula naye.