M'maso mwake munthu woonongeka anyozeka; koma awachitira ulemu akuopa Yehova. Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai.
1 Samueli 19:6 - Buku Lopatulika Ndipo Saulo anamvera mau a Yonatani; nalumbira, Pali Yehova, sadzaphedwa iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Saulo anamvera mau a Yonatani; nalumbira, Pali Yehova, sadzaphedwa iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Saulo adamvera mau a Yonatani, ndipo adalumbira kuti, “Mulungudi! Davideyo sadzaphedwa!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli anamvera mawu a Yonatani ndipo analumbira kuti, “Pali Yehova, Davide sadzaphedwa.” |
M'maso mwake munthu woonongeka anyozeka; koma awachitira ulemu akuopa Yehova. Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai.
Pakuti, pali Yehova wakupulumutsa Israele, chingakhale chili m'mwana wanga Yonatani, koma adzafa ndithu. Koma pakati pa anthu onse panalibe mmodzi wakumyankha iye.
popeza iye anataya moyo wake nakantha Mfilistiyo, ndipo Yehova anachitira Aisraele onse chipulumutso chachikulu, inu munachiona, nimunakondwera; tsono mudzachimwiranji mwazi wosalakwa, ndi kumupha Davide popanda chifukwa?
Pamenepo Yonatani anaitana Davide, namuuza zonsezi. Ndipo Yonatani anafika naye Davide kwa Saulo, iye nakhalanso pamaso pake monga kale.
Ndipo Saulo anamlumbirira kwa Yehova, nati, Pali Yehova, palibe chilango chidzakugwera chifukwa cha chinthu ichi.