1 Samueli 19:19 - Buku Lopatulika Ndipo wina anauza Saulo, kuti, Onani Davide ali ku Nayoti mu Rama. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo wina anauza Saulo, kuti, Onani Davide ali ku Nayoti m'Rama. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Saulo atamva kuti Davide ali ku Nayoti ku Rama, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli anamva kuti, “Davide ali ku Nayoti ku Rama.” |
Chomwecho anathawa Davide, napulumuka, nafika kwa Samuele ku Rama, namuuza zonse Saulo anamchitira. Ndipo iye ndi Samuele anakhala ku Nayoti.
Ndipo Saulo anatumiza mithenga kuti igwire Davide, ndipo pamene inaona gulu la aneneri alikunenera, ndi Samuele mkulu wao alikuimapo, mzimu wa Mulungu unagwera mithenga ya Saulo, ninenera iyonso.
Ndipo a ku Zifi anakwera kwa Saulo ku Gibea, nati, Davide salikubisala kwathu kodi, m'ngaka za m'nkhalango ku Horesi, m'phiri la Hakila, limene lili kumwera kwa chipululu?
Ndipo Azifi anafika kwa Saulo ku Gibea, nati, Kodi Davide sali kubisala m'phiri la Hakila, kupenya kuchipululu!