1 Samueli 19:18 - Buku Lopatulika Chomwecho anathawa Davide, napulumuka, nafika kwa Samuele ku Rama, namuuza zonse Saulo anamchitira. Ndipo iye ndi Samuele anakhala ku Nayoti. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chomwecho anathawa Davide, napulumuka, nafika kwa Samuele ku Rama, namuuza zonse Saulo anamchitira. Ndipo iye ndi Samuele anakhala ku Nayoti. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Davide adathaŵa napulumuka, nakafika kwa Samuele ku Rama. Adafotokozera Samuele zonse zimene Saulo adamuchita. Tsono Davideyo pamodzi ndi Samuele adakakhala ku Nayoti. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Davide anathawa napulumuka. Pambuyo pake anapita kwa Samueli ku Rama nakamuwuza zonse zimene Sauli anamuchita. Kenaka iye ndi Samueli anapita kukakhala ku Nayoti. |
Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.
Ndipo iwo anauka mamawa, nalambira pamaso pa Yehova, nabwerera, nafikanso kwao ku Rama; ndipo Elikana anadziwa mkazi wake Hana, Yehova namkumbukira iye.
Pamenepo Samuele ananka ku Rama; ndi Saulo anakwera kunka kunyumba yake ku Gibea wa Saulo.
Pamenepo iyenso anamuka ku Rama, nafika ku chitsime chachikulu chili ku Seku, nafunsa nati, Samuele ndi Davide ali kuti? Ndipo wina anati, Taonani, ali ku Nayoti mu Rama.
Ndipo anapita komweko ku Nayoti mu Rama; ndi mzimu wa Mulungu unamgwera iyenso; ndipo anapitirira, nanenera, mpaka anafika ku Nayoti mu Rama.
Ndipo Davide anathawa ku Nayoti mu Rama, nadzanena pamaso pa Yonatani, Ndachitanji ine? Kuipa kwanga kuli kotani? Ndi tchimo langa la pamaso pa atate wanu ndi chiyani, kuti amafuna moyo wanga?
Ndipo anyamata a Akisi ananena naye, Uyu si Davide mfumu ya dzikolo kodi? Sanathirirana mang'ombe za iye kodi m'magule ao, ndi kuti, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani?
M'menemo Samuele ndipo atafa, ndipo Aisraele onse atalira maliro ake, namuika mu Rama, m'mzinda mwao. Ndipo Saulo anachotsa m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula onse.
Ndipo anabwera ku Rama, pakuti nyumba yake inali kumeneko; ndipo pamenepo anaweruza Israele; namangapo guwa la nsembe la Yehova.