Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Yonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kunka ku Yerusalemu.
1 Samueli 19:17 - Buku Lopatulika Nati Saulo kwa Mikala, Wandinyengeranji chomwechi, ndi kulola mdani wanga apulumuke? Ndipo Mikala anayankha Saulo, Iye anati kwa ine, Undilole ndipite, ndingakuphe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nati Saulo kwa Mikala, Wandinyengeranji chomwechi, ndi kulola mdani wanga apulumuke? Ndipo Mikala anayankha Saulo, Iye anati kwa ine, Undilole ndipite, ndingakuphe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atamva zimenezi Saulo adafunsa Mikala kuti, “Chifukwa chiyani wandinyenga chotere pa kulola kuti mdani wanga athaŵe?” Mikala adayankha kuti, “Davide adaandiwuza kuti, ‘Undilole ndipite. Ngati sutero, ndikupha.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Sauli anafunsa Mikala kuti, “Nʼchifukwa chiyani wandinamiza chotere polola kuti mdani wanga athawe?” Mikala anayankha kuti, “Davide anandiwuza kuti, ‘Ukapanda kutero ndikupha.’ ” |
Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Yonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kunka ku Yerusalemu.
Ndipo Abinere anabwereza kunena kwa Asahele, Patuka pakunditsata ine. Ndidzakukanthiranji kukugwetsa pansi? Ndikatero ndidzaweramutsanso bwanji nkhope yanga kwa mbale wako Yowabu?
Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kuchita choipacho pamaso pa Yehova.
Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta mu Betelehemu ndi ta m'midzi yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.
Ndipo pakulowa mithengayo, onani, pakama pali chifanizo ndi mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwake.
Mfumu niuza asilikali akuima chomzinga iye, Potolokani, iphani ansembe a Yehova; chifukwa agwirizana ndi Davide, ndipo anadziwa kuti alinkuthawa, koma sanandiululire. Koma anyamata a mfumu sanafune kutambalitsa manja ao kupha ansembe a Yehova.
Ndipo mkaziyo pakuona Samuele, anafuula ndi mau aakulu; ndi mkaziyo analankhula ndi Saulo, nati, Munandinyengeranji? Popeza inu ndinu Saulo.