Ndipo Mikala anatenga terafi namuika pakama, naika mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwake, nachifunda zofunda.
1 Samueli 19:16 - Buku Lopatulika Ndipo pakulowa mithengayo, onani, pakama pali chifanizo ndi mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakulowa mithengayo, onani, pakama pali chifanizo ndi mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthuwo atakaloŵa, adangoona fano pabedipo ndi mtsamiro wa ubweya wambuzi kumutu kwake kwa fanolo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma pamene anthuwo analowa, anangoona fano pa bedipo ndi pilo wa ubweya wa mbuzi ku mutu kwake. |
Ndipo Mikala anatenga terafi namuika pakama, naika mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwake, nachifunda zofunda.
Ndipo Saulo anatumiza mithengayo kuti ikaone Davide, nati, Mumtengere iye pa kama wake, kuti ndidzamuphe.
Nati Saulo kwa Mikala, Wandinyengeranji chomwechi, ndi kulola mdani wanga apulumuke? Ndipo Mikala anayankha Saulo, Iye anati kwa ine, Undilole ndipite, ndingakuphe.