Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 19:13 - Buku Lopatulika

Ndipo Mikala anatenga terafi namuika pakama, naika mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwake, nachifunda zofunda.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Mikala anatenga chifanizo nachiika pakama, naika mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwake, nachifunda zofunda.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mikalayo adatenga fano lam'nyumba naligoneka pa bedi, naika mtsamiro wa ubweya wambuzi kumutu kwake kwa fanolo, nalifunditsa nsalu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kenaka Mikala anatenga fano naligoneka pa bedi nayika pilo wa ubweya wa mbuzi ku mutu kwa fanolo ndipo analifunditsa nsalu.

Onani mutuwo



1 Samueli 19:13
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Labani ananka kukasenga nkhosa zake: ndipo Rakele anaba aterafi a atate wake.


Pakuti ana a Israele adzakhala masiku ambiri opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda choimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi;


Koma munthuyu Mika anali nayo nyumba ya milungu, napanga chovala cha wansembe, ndi aterafi, namninkha zansembe mwana wake wina wamwamuna, amene anakhala wansembe wake.


Pamenepo anayankha amuna asanu anamukawo kukazonda dziko la Laisi, nanena ndi abale ao, Kodi mudziwa kuti m'nyumba izi muli chovala cha wansembe, ndi aterafi ndi fano losema, ndi fano loyenga? Ndipo tsopano dziwani choyenera inu kuchita.


koma amuna asanu omukawo kukazonda dziko anakwera analowako, natenga fano losema, ndi chovala cha wansembe ndi aterafi, ndi fano loyenga; ndi wansembe anaima polowera pa chipata pamodzi ndi amuna mazana asanu ndi limodzi omangira zida za nkhondo m'chuuno.


Ndipo pakulowa mithengayo, onani, pakama pali chifanizo ndi mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwake.