Ndipo iwo anati, Kuona tinaona kuti Yehova ali ndi iwe; ndipo tinati, Tilumbiriranetu tonse awiri, ife ndi iwe, tichite pangano ndi iwe;
1 Samueli 18:28 - Buku Lopatulika Ndipo Saulo anaona, nadziwa kuti Yehova ali ndi Davide; ndi kuti Mikala mwana wa Saulo anamkonda Davide. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Saulo anaona, nadziwa kuti Yehova ali ndi Davide; ndi kuti Mikala mwana wa Saulo anamkonda Davide. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Saulo atazindikira kuti Chauta ali naye Davide, ndiponso kuti mwana wake Mikala ankamkonda Davideyo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli atazindikira kuti Yehova anali ndi Davide ndiponso kuti mwana wake Mikala amamukonda Davide, |
Ndipo iwo anati, Kuona tinaona kuti Yehova ali ndi iwe; ndipo tinati, Tilumbiriranetu tonse awiri, ife ndi iwe, tichite pangano ndi iwe;
Ndipo Labani anati kwa iye, Ngatitu ndikapeza ufulu pamaso pako, ukhale, chifukwa ndazindikira kuti Yehova wandidalitsa ine chifukwa cha iwe.
Ndipo mbuyake anaona kuti Yehova anali ndi iye, ndi kuti Yehova anamlemereza m'dzanja lake zonse anazichita.
Taona, ndikupatsa ena otuluka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.
Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anakonda Davide; ndipo pakumva Saulo, anakondwera nako.
Ndipo asanathe masikuwo, ananyamuka Davide, ndi anthu ake, nakaphako Afilisti mazana awiri, ndipo Davide anatenga nsonga za makungu ao nazipatsa mofikira kwa mfumu, kuti akhale mkamwini wa mfumu. Ndipo Saulo anampatsa Mikala mwana wake wamkazi akhale mkazi wake.
Ndipo tsono taona ndidziwa kuti udzakhala mfumu ndithu, ndi kuti ufumu wa Israele udzakhazikika m'dzanja lako.
Pomwepo Saulo anati kwa Davide, Udalitsike iwe, mwana wanga Davide; udzachita ndithu champhamvu, nudzapambana. Chomwecho Davide anamuka, ndipo Saulo anabwera kwao.