Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.
1 Samueli 18:22 - Buku Lopatulika Ndipo Saulo analamulira anyamata ake, nati, Mulankhule naye Davide m'tseri, ndi kuti, Taonani mfumu akondwera nanu, ndi anyamata ake onse akukondani; chifukwa chake tsono, khalani mkamwini wa mfumu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Saulo analamulira anyamata ake, nati, Mulankhule naye Davide m'tseri, ndi kuti, Taonani mfumu akondwera nanu, ndi anyamata ake onse akukondani; chifukwa chake tsono, khalani mkamwini wa mfumu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero adalamula nduna zake kuti, “Mulankhule naye Davide pambali nkumuuza kuti, ‘Mfumu imakukonda, ndipo ngakhale nduna zake zimakukonda. Tsono ukhale mkamwini wa mfumu.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli analamulanso nduna zake kuti, “Muyankhuleni Davide mwamseri ndi kumuwuza kuti, ‘Taona, mfumu imakondwera nawe, ndipo nduna zake zonse zimakukonda. Tsono ukhale mkamwini wa mfumu.’ ” |
Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.
Nati Saulo, Ndidzampatsa iye, kuti amkhalire msampha, ndi kuti dzanja la Afilisti limgwere. Chifukwa chake Saulo ananena ndi Davide, Lero udzakhala mkamwini wanga kachiwiri.
Ndipo anyamata a Saulo analankhula mau awa m'makutu a Davide. Nati Davide, Kodi muchiyesera chinthu chopepuka kukhala mkamwini wa mfumu, popeza ndili munthu wosauka, ndi wopeputsidwa.