Masiku anapitawo, pamene Saulo anali mfumu yathu, inu ndinu amene munatsogolera Aisraele kutuluka nao ndi kubwera nao; ndipo Yehova ananena nanu, Uzidyetsa anthu anga Israele, ndi kukhala mtsogoleri wa Israele.
1 Samueli 18:16 - Buku Lopatulika Koma Aisraele onse ndi Ayuda onse anamkonda Davide pakuti anawatsogolera kutuluka ndi kulowa nao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Aisraele onse ndi Ayuda onse anamkonda Davide pakuti anawatsogolera kutuluka ndi kulowa nao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma anthu onse a ku Israele ndi a ku Yuda ankamkonda Davide, chifukwa iyeyu ankaŵatsogolera namapambana pa zonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Aisraeli onse ndi anthu a Yuda ankamukonda Davide chifukwa ankawatsogolera pa nkhondo zawo. |
Masiku anapitawo, pamene Saulo anali mfumu yathu, inu ndinu amene munatsogolera Aisraele kutuluka nao ndi kubwera nao; ndipo Yehova ananena nanu, Uzidyetsa anthu anga Israele, ndi kukhala mtsogoleri wa Israele.
Ndipo tsopano, Yehova Inu Mulungu wanga, mwalonga ine kapolo wanu ufumu m'malo mwa atate wanga Davide, koma ine ndine kamwana, sindidziwa kutuluka kapena kulowa.
Pakuti Mordekai Myuda anatsatana naye mfumu Ahasuwero, nakhala wamkulu mwa Ayuda, navomerezeka mwa unyinji wa abale ake wakufunira a mtundu wake zokoma, ndi wakunena za mtendere kwa mbeu yake yonse.
wakutuluka pamaso pao, ndi kulowa pamaso pao, wakuwatulutsa ndi kuwalowetsa; kuti khamu la Yehova lisakhale ngati nkhosa zopanda mbusa.
Ndipo alembi ndi ansembe aakulu anafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo anaopa anthu; pakuti anazindikira kuti ananenera pa iwo fanizo ili.
Chifukwa chake Saulo anamchotsa kuti asakhale naye, namuika akhale mtsogoleri wake wa anthu chikwi chimodzi; ndipo iye anatsogolera anthu kutuluka ndi kubwera nao.
Ndipo Davide anatuluka kunka kulikonse Saulo anamtumako, nakhala wochenjera; ndipo Saulo anamuika akhale woyang'anira anthu a nkhondo; ndipo ichi chinakomera anthu onse, ndi anyamata a Saulo omwe.