Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa; adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa.
1 Samueli 18:15 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Saulo anaona kuti analikukhala wochenjera ndithu anamuopa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Saulo anaona kuti analikukhala wochenjera ndithu anamuopa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono pamene Saulo adaona kuti Davide akupambana kwambiri, adayamba kuchita naye mantha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli ataona momwe Davide ankapambanira, iye anamuopa kwambiri. |
Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa; adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa.
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.
Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso.
Koma Aisraele onse ndi Ayuda onse anamkonda Davide pakuti anawatsogolera kutuluka ndi kulowa nao.