Ndipo Saulo anati kwa Davide, Sukhoza iwe kukomana ndi Mfilisti uyu kukaponyana naye; pakuti iwe ndiwe mnyamata, koma iye anazolowera nkhondo kuyambira ubwana wake.
1 Samueli 17:56 - Buku Lopatulika Ndipo mfumu inati, Ufunsire kuti mnyamatayo ndi mwana wa yani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumu inati, Ufunsire kuti mnyamatayo ndi mwana wa yani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo mfumu idati, “Kafunse kuti kodi mnyamata ameneyu ndi mwana wa yani?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumu inati, “Pita kafufuze kuti mnyamata ameneyu ndi mwana wa yani.” |
Ndipo Saulo anati kwa Davide, Sukhoza iwe kukomana ndi Mfilisti uyu kukaponyana naye; pakuti iwe ndiwe mnyamata, koma iye anazolowera nkhondo kuyambira ubwana wake.
Ndipo pamene Saulo anaona Davide alikutulukira kwa Mfilistiyo, iye anati kwa Abinere, kazembe wa khamu la nkhondo, Abinere, mnyamata uyu ndi mwana wa yani? Nati Abinere, Pali moyo wanu, mfumu, ngati ndidziwa.
Ndipo pamene Davide anabwera, atapha Mfilistiyo, Abinere anamtenga, nafika naye pamaso pa Saulo, mutu wa Mfilistiyo uli m'dzanja lake.