Nati iye, Chinkana atulukira mumtendere, agwireni amoyo; chinkana atulukira m'nkhondo, agwireni, amoyo.
1 Samueli 17:42 - Buku Lopatulika Ndipo Mfilisti pakumwazamwaza maso, ndi kuona Davide, anampeputsa; popeza anali mnyamata chabe, wofiirira, ndi wa nkhope yokongola. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mfilisti pakumwazamwaza maso, ndi kuona Davide, anampeputsa; popeza anali mnyamata chabe, wofiirira, ndi wa nkhope yokongola. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo atayang'ana Davideyo, adayamba kumnyoza, poona kuti anali mnyamata chabe, wofiirira ndiponso wa maonekedwe okongola. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfilisitiyo atangomuona Davide, anamunyoza popeza kuti Davide anali mnyamata chabe wofiirira ndi wa maonekedwe abwino. |
Nati iye, Chinkana atulukira mumtendere, agwireni amoyo; chinkana atulukira m'nkhondo, agwireni, amoyo.
Ndipo anatumiza munthu, nabwera naye. Tsono iye anali wofiirira, ndi wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma. Ndipo Yehova anati, Nyamuka umdzoze, pakuti ndi ameneyu.
Ndipo Saulo anati kwa Davide, Sukhoza iwe kukomana ndi Mfilisti uyu kukaponyana naye; pakuti iwe ndiwe mnyamata, koma iye anazolowera nkhondo kuyambira ubwana wake.
Ndipo Mfilistiyo anadza, nayandikira kwa Davide; ndi wonyamula chikopa chake anamtsogolera.