Koma ndidzachitira chifundo nyumba ya Yuda, ndi kuwapulumutsa mwa Ine Yehova Mulungu wao, osawapulumutsa ndi uta, kapena lupanga, kapena nkhondo ndi akavalo, kapena apakavalo.
1 Samueli 17:39 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anamanga lupanga lake pamwamba pa zovala zake, nayesa kuyenda nazo; popeza sanaziyesere kale. Ndipo Davide anati kwa Saulo, Sindingathe kuyenda ndi izi; pakuti sindinazizolowere. Nazivula Davide. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anamanga lupanga lake pamwamba pa zovala zake, nayesa kuyenda nazo; popeza sanaziyesera kale. Ndipo Davide anati kwa Saulo, Sindikhoza kuyenda ndi izi; pakuti sindinazizolowera. Nazivula Davide. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka Davide adamanga lupanga m'chiwuno mwake. Atayesera kuyenda, adaona kuti akulephera poti sadazoloŵere. Ndiye adauza Saulo kuti, “Sindingathe kuyenda nazo, poti sindidazoloŵere.” Choncho adavula zovalazo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anamangirira lupanga pa mwinjirowo. Atayesa kuyenda nazo, analephera chifukwa anali asanazizolowere. Iye anati kwa Sauli, “Sindingathe kuyenda nazo chifukwa sindinazizolowere.” Ndipo anazivula. |
Koma ndidzachitira chifundo nyumba ya Yuda, ndi kuwapulumutsa mwa Ine Yehova Mulungu wao, osawapulumutsa ndi uta, kapena lupanga, kapena nkhondo ndi akavalo, kapena apakavalo.
Pamenepo anayankha, nanena kwa ine, ndi kuti, Awa ndi mau a Yehova kwa Zerubabele, Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.
Ndipo Saulo anaveka Davide zovala zake za iye yekha, namveka chisoti chamkuwa pamutu pake, namvekanso malaya aunyolo.
Natenga ndodo yake m'dzanja lake nadzisankhira miyala isanu yosalala ya mumtsinje, naiika m'thumba la kubusa, limene anali nalo ndilo chibete; ndi choponyera miyala chinali m'dzanja lake, momwemo anayandikira kwa Mfilistiyo.