Mangani akavalo, bwerani, inu apakavalo, imani ndi zisoti zazitsulo; tuulani nthungo zanu, valani malaya achitsulo.
1 Samueli 17:38 - Buku Lopatulika Ndipo Saulo anaveka Davide zovala zake za iye yekha, namveka chisoti chamkuwa pamutu pake, namvekanso malaya aunyolo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Saulo anaveka Davide zovala zake za iye yekha, namveka chisoti chamkuwa pamutu pake, namvekanso malaya aunyolo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Saulo adaveka Davide zovala zake zankhondo. Adamveka chisoti chamkuŵa ndi malaya achitsulo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Sauli anamveka Davide mwinjiro wake. Anamuveka zovala zankhondo ndi chipewa cha mkuwa. |
Mangani akavalo, bwerani, inu apakavalo, imani ndi zisoti zazitsulo; tuulani nthungo zanu, valani malaya achitsulo.
Nati Davide, Yehova wakundipulumutsa pa mphamvu ya mkango, ndi mphamvu ya chimbalangondo, Iyeyu adzandipulumutsa m'dzanja la Mfilisti uyu. Ndipo Saulo anati kwa Davide, Muka, Yehova akhale nawe.
Ndipo Davide anamanga lupanga lake pamwamba pa zovala zake, nayesa kuyenda nazo; popeza sanaziyesere kale. Ndipo Davide anati kwa Saulo, Sindingathe kuyenda ndi izi; pakuti sindinazizolowere. Nazivula Davide.
Ndipo Yonatani anavula malaya ake anali nao, napatsa Davide, ndi zovala zake, ngakhale lupanga lake, ndi uta wake, ndi lamba lake.