Chimene chinazomoledwa ndi chilombo sindinachitengere kwa iwe; ndekha ndinalipira; padzanja langa unachifuna, chingakhale chobedwa kapena pausiku kapena pausana.
1 Samueli 17:34 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anati kwa Saulo, Ine kapolo wanu ndinalikusunga nkhosa za atate wanga; ndipo pakubwera mkango, mwina chimbalangondo ndi kutenga nkhosa ya gululo, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anati kwa Saulo, Ine kapolo wanu ndinalikusunga nkhosa za atate wanga; ndipo pakubwera mkango, mwina chimbalangondo ndi kutenga nkhosa ya gululo, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Davide adauza Saulo kuti, “Mnyamata wanune ndinkaŵeta nkhosa za bambo wanga. Ndipo mkango ukafika, kapena chimbalangondo, ndi kugwira mwanawankhosa pakati pa nkhosazo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Davide anati kwa Sauli, “Kapolo wanune ndinkaweta nkhosa za abambo anga. Ndipo mkango kapena chimbalangondo chikamabwera ndi kugwira mwana wankhosa pakati pa nkhosazo, |
Chimene chinazomoledwa ndi chilombo sindinachitengere kwa iwe; ndekha ndinalipira; padzanja langa unachifuna, chingakhale chobedwa kapena pausiku kapena pausana.
Husai anatinso, Mudziwa atate wanu ndi anthu ake kuti ndizo ngwazi, ndipo ali ndi mitima yowawa monga chimbalangondo chochilanda ana ake kuthengo; ndipo atate wanu ali munthu wodziwa nkhondo, sadzagona pamodzi ndi anthu.
Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabizeeli amene anachita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Mowabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m'mbuna nyengo ya chipale chofewa;
Benaya mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi ya ku Kabizeeli, wochita zachikulu, anapha ana awiri a Ariyele wa ku Mowabu; anatsikanso, napha mkango m'kati mwa dzenje nyengo ya chipale chofewa.
Ndikumbukira masiku a kale lomwe; zija mudazichita ndilingirirapo; ndikamba pandekha za ntchito ya manja anu.
Monga mbusa afunafuna nkhosa zake tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zake zobalalika, momwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m'malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.
Atero Yehova, Monga mbusa alanditsa m'kamwa mwa mkango miyendo iwiri, kapena kansonga ka khutu, momwemo adzalanditsidwa ana a Israele okhala pansi mu Samariya, m'ngodya ya guwa logonapo, ndi pa mitsamiro ya kama.
Pakuti taonani, ndidzautsa mbusa m'dziko amene sadzazonda otayika, kapena kufunafuna zomwazika, kapena kulunzitsa yothyoka, kapena kudyetsa yamoyo, koma adzadya nyama ya zonenepa, nadzang'amba ziboda zao.
Ndipo ndidzachotsa mwazi wake m'kamwa mwake, ndi zonyansa zake pakati pa mano ake; momwemo iyenso adzakhala wotsalira wa Mulungu wathu, ndipo adzakhala ngati mkulu wa fuko mu Yuda, ndi Ekeroni ngati Myebusi.
amene mwa chikhulupiriro anagonjetsa maufumu, anachita chilungamo, analandira malonjezano, anatseka pakamwa pa mikango,
Ndipo chilombo ndinachionacho chinafanana ndi nyalugwe, ndi mapazi ake ngati mapazi a chimbalangondo, ndi pakamwa pake ngati pakamwa pa mkango; ndipo chinjoka chinampatsa iye mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu.
Ndipo unamgwera iye kolimba mzimu wa Yehova, naung'amba monga akadang'amba mwanawambuzi, wopanda kanthu m'dzanja lake; koma sanauze atate wake kapena amai wake chimene adachichita.
Koma Davide akamuka kwa Saulo, nabwerera kudzadyetsa nkhosa za atate wake ku Betelehemu.
Ndipo Saulo anati kwa Davide, Sukhoza iwe kukomana ndi Mfilisti uyu kukaponyana naye; pakuti iwe ndiwe mnyamata, koma iye anazolowera nkhondo kuyambira ubwana wake.
ndinachithamangira, ndi kuchikantha, ndi kuitulutsa m'kamwa mwake; ndipo pamene chinandiukira, ndinagwira tchowa lake ndi kuchikantha ndi kuchipha.