1 Samueli 17:29 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anati, Ndachitanji tsopano? Palibe chifukwa kodi? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anati, Ndachitanji tsopano? Palibe chifukwa kodi? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide adati, “Kodi ndachimwa chiyani? Ndiye kuti ndileke nkulankhula komwe?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anati, “Kodi ndachita chiyani ine? Kodi ndisamayankhule?” |
osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.
Ndipo Eliabu mkulu wake anamumva iye alikulankhula ndi anthu; ndipo Eliyabu anapsa mtima ndi Davide, nati, Unatsikiranji kuno? Ndi nkhosa zija zowerengeka unazisiya ndi yani, m'chipululu muja? Ine ndidziwa kudzikuza kwako ndi kuipa kwa mtima wako; pakuti watsika kuti udzaone nkhondoyi.
Napotolokera iye kwa munthu wina, nalankhula mau omwewo; ndipo anthu anamyankhanso monga momwemo.