Ndipo anthuwo anamyankha motero, nati, Adzamchitira munthu wakumupha iye mwakutimwakuti.
Anthu adamuuzanso zomwe zija zimene mfumu idaati idzachitire munthu wodzapha Goliyatiyo.
Anthu anamuwuzanso zonse zimene mfumu inanena kuti idzachitira munthu amene adzapha Mfilisitiyo.
Nati Aisraele, Kodi mwaona munthu uyu amene anakwera kuno? Zoonadi iye anakwera kuti adzanyoze Israele, ndipo munthu wakumupha iye, mfumu idzamlemeretsa ndi chuma chambiri, nidzampatsa mwana wake wamkazi, nidzayesa nyumba ya atate wake yaufulu mu Israele.
Napotolokera iye kwa munthu wina, nalankhula mau omwewo; ndipo anthu anamyankhanso monga momwemo.