Chikwi chimodzi chidzathawa pakuwadzudzula mmodzi; pakukudzudzulani anthu asanu mudzathawa; kufikira inu mudzasiyidwa ngati mlongoti pamwamba paphiri, ndi ngati mbendera pamwamba pa chitunda.
1 Samueli 17:24 - Buku Lopatulika Ndipo Aisraele onse, pakumuona munthuyo, anamthawa, naopa kwambiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Aisraele onse, pakumuona munthuyo, anamthawa, naopa kwambiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aisraele onse atamuwona munthuyo, adathaŵa chifukwa ankamuwopa kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aisraeli ataona munthuyo, anamuthawa ndi mantha aakulu. |
Chikwi chimodzi chidzathawa pakuwadzudzula mmodzi; pakukudzudzulani anthu asanu mudzathawa; kufikira inu mudzasiyidwa ngati mlongoti pamwamba paphiri, ndi ngati mbendera pamwamba pa chitunda.
Ndipo anauza a nyumba ya Davide, kuti Aramu wapangana ndi Efuremu. Ndipo mtima wake unagwedezeka, ndi mtima wa anthu ake, monga mitengo ya m'nkhalango igwedezeka ndi mphepo.
Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.
Tinaonakonso Anefili, ana a Anaki, obadwa ndi Anefili; ndipo tinaoneka m'maso mwathu ngati ziwala; momwemonso tinaoneka m'maso mwao.
Mmodzi akadapirikitsa zikwi, awiri akadathawitsa zikwi khumi, akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao, akadapanda kuwapereka Yehova.
Ndipo pamene Saulo ndi Aisraele onse anamva mau ao a Mfilistiyo, anadodoma, naopa kwambiri.
Ndipo m'mene iye anali chilankhulire nao, onani chinakwerako chiwindacho, Mfilisti wa ku Gati, dzina lake Goliyati, wotuluka pakati pa mipambo ya Afilisti, nalankhula monga mau omwe aja; ndipo Davide anawamva.
Nati Aisraele, Kodi mwaona munthu uyu amene anakwera kuno? Zoonadi iye anakwera kuti adzanyoze Israele, ndipo munthu wakumupha iye, mfumu idzamlemeretsa ndi chuma chambiri, nidzampatsa mwana wake wamkazi, nidzayesa nyumba ya atate wake yaufulu mu Israele.