Ndipo Samuele anati kwa Yese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng'ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samuele anati kwa Yese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno.
1 Samueli 17:15 - Buku Lopatulika Koma Davide akamuka kwa Saulo, nabwerera kudzadyetsa nkhosa za atate wake ku Betelehemu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Davide akamuka kwa Saulo, nabwerera kudzadyetsa nkhosa za atate wake ku Betelehemu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Davide ankapita ku zithando za Saulo, namabwerako nthaŵi zina kukaŵeta nkhosa za bambo wake ku Betelehemu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Davide ankapita ku misasa ya Sauli ndi kubwerako kuti azikaweta nkhosa za abambo ake ku Betelehemu. |
Ndipo Samuele anati kwa Yese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng'ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samuele anati kwa Yese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno.
Ndipo Davide anati kwa Saulo, Ine kapolo wanu ndinalikusunga nkhosa za atate wanga; ndipo pakubwera mkango, mwina chimbalangondo ndi kutenga nkhosa ya gululo,