Tsono inu mbuye wathu muuze anyamata anu, amene ali pamaso panu, kuti afune munthu wanthetemya wodziwa kuimba zeze; ndipo kudzakhala, pamene mzimu woipa wochokera kwa Mulungu uli pa inu, iyeyo adzaimba ndi dzanja lake, ndipo mudzakhala wolama.
1 Samueli 16:17 - Buku Lopatulika Ndipo Saulo anati kwa anyamata ake, Mundifunire tsono munthu wakudziwa kuimba bwino, nimubwere naye kwa ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Saulo anati kwa anyamata ake, Mundifunire tsono munthu wakudziwa kuimba bwino, nimubwere naye kwa ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Saulo adaŵauza kuti, “Chabwino mundifunire munthu wodziŵa bwino kuimba kwake, ndipo mubwere naye kuno.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Sauli anati kwa atumiki ake, “Chabwino, kandipezereni munthu wodziwa bwino kuyimba ndipo mubwere naye kuno.” |
Tsono inu mbuye wathu muuze anyamata anu, amene ali pamaso panu, kuti afune munthu wanthetemya wodziwa kuimba zeze; ndipo kudzakhala, pamene mzimu woipa wochokera kwa Mulungu uli pa inu, iyeyo adzaimba ndi dzanja lake, ndipo mudzakhala wolama.
Ndipo mnyamata wake wina anayankha, nati, Taonani, ine ndaona mwana wa Yese wa ku Betelehemu, ndiye wanthetemya wodziwa kuimbira, ndipo ali wa mtima wolimba ndi woyenera nkhondo, ndiponso ali wochenjera manenedwe ake; ndiye munthu wokongola, ndipo Yehova ali naye.