Ndipo Samuele anati kwa Yese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng'ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samuele anati kwa Yese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno.
1 Samueli 16:10 - Buku Lopatulika Ndipo Yese anapititsapo ana ake aamuna asanu ndi awiri. Koma Samuele anati kwa Yese, Yehova sanawasankhe awa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yese anapititsapo ana ake amuna asanu ndi awiri. Koma Samuele anati kwa Yese, Yehova sanawasankhe awa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Yese adatumiza ana ake aamuna asanu ndi aŵiri kuti apite kwa Samuele. Koma Samueleyo adati, “Chauta sadaŵasankhe ameneŵa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pambuyo pake, Yese anayitana ana ake amuna asanu ndi awiri kuti apite kwa Samueli. Koma Samueli anati, “Yehova sanasankhe amenewa.” |
Ndipo Samuele anati kwa Yese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng'ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samuele anati kwa Yese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno.
Tsono Davide anali mwana wa Mwefurati uja wa ku Betelehemu ku Yuda, dzina lake ndiye Yese; ameneyu anali nao ana aamuna asanu ndi atatu; ndipo m'masiku a Saulo munthuyo anali nkhalamba, mwa anthu.