Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 15:32 - Buku Lopatulika

Ndipo Samuele anati, Bwerani naye kwa ine kuno Agagi mfumu ya Aamaleke. Ndipo Agagi anabwera kwa iye mokondwera. Nati Agagi, Zoonadi kuwawa kwa imfa kunapitirira.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Samuele anati, Bwerani naye kwa ine kuno Agagi mfumu ya Aamaleke. Ndipo Agagi anabwera kwa iye mokondwera. Nati Agagi, Zoonadi kuwawa kwa imfa kunapitirira.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pambuyo pake Samuele adauza Saulo kuti, “Bwera nayeni kuno Agagi uja, mfumu ya Aamaleke.” Ndipo Agagiyo adafika kwa Samuele mokondwa, chifukwa adati, “Ndithudi, zoŵaŵa za imfa zapita!”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kenaka Samueli anati, “Bwera nayeni kuno Agagi, mfumu ya Amaleki ija.” Choncho Agagi anapita kwa Samueli mokondwa chifukwa ankaganiza kuti, “Ndithu zowawa za imfa zapita.”

Onani mutuwo



1 Samueli 15:32
8 Mawu Ofanana  

Ndipo iye wakuthawa chifukwa cha mantha adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'dzenje adzagwidwa m'khwekhwe; pakuti ndidzatengera pa iye, pa Mowabu, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.


Chifukwa chake ndawalikha mwa aneneri; ndawapha ndi mau a pakamwa panga; ndi maweruzo anga atuluka ngati kuunika.


Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.


Pamenepo Yoswa anati, Tsegula pakamwa pa phanga ndi kunditulutsira m'phanga mafumu asanuwo.


Monga momwe unadzichitira ulemu, nudyerera, momwemo muuchitire chouzunza ndi chouliritsa maliro: pakuti unena mumtima mwake, Ndikhala ine mfumu, wosati wamasiye ine, wosaona maliro konse ine.


Ndipo Gideoni anakwerera njira ya iwo okhala m'mahema kum'mawa kwa Noba, ndi Yogobeha, nakantha khamulo popeza khamulo linakhala lokhazikika mtima.


Chomwecho Samuele anabwerera natsata Saulo; ndi Saulo analambira Yehova.


Ndipo Samuele anati, Monga lupanga lako linachititsa akazi ufedwa, momwemo mai wako adzakhala mfedwa mwa akazi. Ndipo Samuele anamdula Agagi nthulinthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.