Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi chipambano, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi padziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.
1 Samueli 15:29 - Buku Lopatulika Ndiponso Wamphamvu wa Israele sanama kapena kulapa; popeza Iye sali munthu kuti akalapa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiponso Wamphamvu wa Israele sanama kapena kulapa; popeza Iye sali munthu kuti akalapa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu Waulemerero wa Aisraele sanama kapena kusintha maganizo. Pakuti Iye si munthu, kuti athe kusintha maganizo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu wa ulemerero wa Israeli sanama kapena kusintha maganizo ake; pakuti iye si munthu, kuti asinthe maganizo ake.” |
Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi chipambano, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi padziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.
Inu Mulungu, ndinu woopsa m'malo oyera anu; Mulungu wa Israele ndiye amene apatsa anthu ake mphamvu ndi chilimbiko. Alemekezeke Mulungu.
Koma mwa Yehova yekha, wina adzati kwa Ine, muli chilungamo ndi mphamvu; ngakhale kwa Iyeyo anthu adzafika, ndi onse amene anamkwiyira, adzakhala ndi manyazi.
Ine Yehova ndachinena, chidzachitika; ndipo ndidzachichita, sindidzamasula, kapena kulekerera, kapena kuwaleka, monga mwa njira zako, ndi monga umo unachitira adzakuweruza iwe, ati Ambuye Yehova.
Ndipo Yehova adzadzuma ali ku Ziyoni, ndi kumveketsa mau ake ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu adzakhala chopulumukirako anthu ake, ndi linga la ana a Israele.
Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?
Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa mu ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m'mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.
Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako; ndi pansipo pali manja osatha. Ndipo aingitsa mdani pamaso pako, nati, Ononga.
ngati tikhala osakhulupirika, Iyeyu akhala wokhulupirika; pakuti sangathe kudzikana yekha.
m'chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthawi zosayamba;
kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;
koma Iye ndi lumbiro mwa Iye amene anenana kwa Iye, Walumbira Ambuye ndipo sadzalapa, iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha).