Ndipo anati mwamunayo, Mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya.
1 Samueli 15:21 - Buku Lopatulika Koma anthuwo anatengako zowawanya, nkhosa ndi ng'ombe, zoposa za zija tidayenera kuziononga, kuziphera nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma anthuwo anatengako zowawanya, nkhosa ndi ng'ombe, zoposa za zija tidayenera kuziononga, kuziphera nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma pa zofunkha anthu adatengako nkhosa ndi ng'ombe, ndi zina zabwino kwambiri, zimene zinkayenera kuwonongedwa, kuti akazipereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wanu, ku Giligala.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma pa zofunkhazo anthu anatengapo nkhosa, ngʼombe ndi zabwino zina zoyenera kuwonongedwa kuti akapereke ngati nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala.” |
Ndipo anati mwamunayo, Mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya.
Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Chiyani chimene wachitachi? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.
Ndipo Saulo anati, Anazitenga kwa Aamaleke; pakuti anthu anasunga nkhosa zokometsetsa ndi ng'ombe, kuzipereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu; koma zina tinaziononga konsekonse.