Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 15:19 - Buku Lopatulika

Chifukwa ninji tsono simunamvere mau a Yehova, koma munathamangira zowawanya, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chifukwa ninji tsono simunamvera mau a Yehova, koma munathamangira zowawanya, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chifukwa chiyani nanga simudamvere mau a Chauta? Chifukwa chiyani mudathamangira zofunkha ndi kuchita zoipira Chauta?”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chifukwa chiyani simunamvere mawu a Yehova? Chifukwa chiyani munathamangira zofunkha ndi kuchita choyipira Yehova?”

Onani mutuwo



1 Samueli 15:19
11 Mawu Ofanana  

Chifukwa ninji unapeputsa mau a Yehova ndi kuchita chimene chili choipa pamaso pake? Unakantha Uriya Muhiti ndi lupanga ndi kutenga mkazi wake akhale mkazi wako; ndipo unamupha iye ndi lupanga la ana a Amoni.


Nachita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawachotsa m'dziko mwao pamaso pa ana a Israele.


Anapititsanso ana ake pamoto m'chigwa cha ana a Hinomu, naombeza maula, nasamalira malodza, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openduza; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.


nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wake; sanadzichepetse kwa Yeremiya mneneri wakunena zochokera pakamwa pa Yehova.


Wopindula monyenga avuta nyumba yake; koma wakuda mitulo adzakhala ndi moyo.


Kodi nyumba ino, imene itchedwa dzina langa, ikhala phanga la okwatula pamaso panu? Taona, Ine ndachiona, ati Yehova.


Ndipo Mose anati, Mutero chifukwa ninji kulakwira mau a Yehova, popeza simudzapindula nako?


pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi, napita ku Tesalonika; Kresike ku Galatiya, Tito ku Dalamatiya.


Ndipo anthuwo anathamangira zowawanyazo, natenga nkhosa, ndi ng'ombe, ndi anaang'ombe, naziphera pansi; anthu nazidya zili ndi mwazi wao.


Ndipo Saulo ananena ndi Samuele, Koma ndinamvera mau a Yehova, ndipo ndinayenda njira Yehova anandituma ine, ndipo ndinabwera naye Agagi mfumu ya Amaleke, ndi Aamaleke ndinawaononga konsekonse.