Pamene Efuremu analankhula panali kunjenjemera; anadzikweza mu Israele; koma pamene anapalamula mwa Baala, anafa.
1 Samueli 15:17 - Buku Lopatulika Nati Samuele, M'mene munali wamng'ono m'maso a inu nokha, kodi simunaikidwe mutu wa mafuko a Israele? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nati Samuele, M'mene munali wamng'ono m'maso a inu nokha, kodi simunaikidwa mutu wa mafuko a Israele? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Samuele adati, “Ngakhale kale munali wamng'ono pamaso pa anthu, tsopano mwasanduka mtsogoleri wa mafuko onse a Aisraele. Chauta adakudzozani kuti mukhale mfumu yomalamulira Aisraele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Apo Samueli anati, “Munali wamngʼono pa maso pa anthu, koma tsopano mwasanduka mtsogoleri wa mafuko a Israeli. Yehova anakudzozani kuti mukhale mfumu yolamulira Aisraeli. |
Pamene Efuremu analankhula panali kunjenjemera; anadzikweza mu Israele; koma pamene anapalamula mwa Baala, anafa.
Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba.
Ndipo anati kwa Iye, Ha! Mbuye, ndidzapulumutsa Israele ndi chiyani? Taonani, banja langa lili loluluka mu Manase, ndipo ine ndine wamng'ono m'nyumba ya atate wanga.
Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?
Chifukwa chake anaonjeza kufunsa Yehova, Watsala wina kodi woyenera kubwera kuno? Ndipo Yehova anati, Onani, alikubisala pakati pa akatundu.
Pomwepo Samuele ananena ndi Saulo, Imani, ndidzakudziwitsani chimene Yehova wanena ndi ine usiku walero. Ndipo iyeyo anati kwa iye, Nenani.
Ndipo Saulo anayankha nati, Sindili Mbenjamini kodi wa fuko laling'ono mwa Israele? Ndiponso banja lathu nlochepa pakati pa mabanja onse a fuko la Benjamini? Potero mulankhula bwanji mau otere ndi ine?