Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 15:14 - Buku Lopatulika

Ndipo Samuele anati, Koma tsono kulirako kwa nkhosa ndilikumva m'makutu anga, ndi kulirako kwa ng'ombe ndilikumva, nchiyani?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Samuele anati, Koma tsono kulirako kwa nkhosa ndilikumva m'makutu anga, ndi kulirako kwa ng'ombe ndilikumva, nchiyani?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma Samuele adati, “Nanga bwanji ndikumva nkhosa ndi ng'ombe zikulira?”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma Samueli anati, “Nanga bwanji ndikumva kulira kwa nkhosa ndi ngʼombe?”

Onani mutuwo



1 Samueli 15:14
11 Mawu Ofanana  

Pakuti adzidyoletsa yekha m'kuona kwake, kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho.


Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakuchitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukulu kotere?


Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula chimene sindinachiike, ndi wotuta chimene sindinachifese;


Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;


Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.


Ndipo Saulo anati, Anazitenga kwa Aamaleke; pakuti anthu anasunga nkhosa zokometsetsa ndi ng'ombe, kuzipereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu; koma zina tinaziononga konsekonse.