ndi dzina la mkazi wa Saulo ndi Ahinowamu mwana wa Ahimaazi; ndi dzina la kazembe wa khamu lankhondo lake ndiye Abinere mwana wa Nere, mbale wake wa atate wa Saulo.
1 Samueli 14:51 - Buku Lopatulika Ndipo atate wa Saulo ndiye Kisi; ndipo Nere atate wa Abinere ndiye mwana wa Abiyele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo atate wa Saulo ndiye Kisi; ndipo Nere atate wa Abinere ndiye mwana wa Abiyele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kisi bambo wa Saulo ndipo Nere bambo wa Abinere, anali ana a Abiyele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kisi abambo a Sauli ndi Neri abambo a Abineri anali ana a Abieli. |
ndi dzina la mkazi wa Saulo ndi Ahinowamu mwana wa Ahimaazi; ndi dzina la kazembe wa khamu lankhondo lake ndiye Abinere mwana wa Nere, mbale wake wa atate wa Saulo.
Ndipo Davide ananyamuka nafika pamalo paja Saulo anamangapo; ndipo Davide adaona pogona Saulo, ndi Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu lake; ndipo Saulo anagona pakati pa linga la magaleta, ndipo anthu adamanga zithando pomzinga pake.
Ndipo panali munthu Mbenjamini, dzina lake ndiye Kisi, mwana wa Abiyele, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, mwana wa Mbenjamini, ndiye ngwazi.
Ndipo Saulo anayankha nati, Sindili Mbenjamini kodi wa fuko laling'ono mwa Israele? Ndiponso banja lathu nlochepa pakati pa mabanja onse a fuko la Benjamini? Potero mulankhula bwanji mau otere ndi ine?