Uta wa Yonatani sunabwerere, ndipo lupanga la Saulo silinabwerere chabe, pa mwazi wa ophedwa, pa mafuta a amphamvuwo.
1 Samueli 14:48 - Buku Lopatulika Ndipo iye anakula mphamvu, nakantha Aamaleke, napulumutsa Aisraele m'manja a akuwawawanya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anakula mphamvu, nakantha Aamaleke, napulumutsa Aisraele m'manja a akuwawawanya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adachita zamphamvu, ndipo adagonjetsa Aamaleke. Motero adapulumutsa Aisraele kwa anthu amene ankaŵalanda zinthu zao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anachita nkhondo mwamphamvu ndi kugonjetsa Aamaleki. Choncho anapulumutsa Aisraeli mʼmanja mwa anthu amene ankawalanda zinthu zawo. |
Uta wa Yonatani sunabwerere, ndipo lupanga la Saulo silinabwerere chabe, pa mwazi wa ophedwa, pa mafuta a amphamvuwo.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ichi m'buku, chikhale chikumbutso, nuchimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse chikumbukiro cha Amaleke pansi pa thambo.
Ndipo kudzali, pamene Yehova Mulungu wanu atakupumulitsirani adani anu onse ozungulira, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanuchanu, kuti muzifafaniza chikumbutso cha Amaleke pansi pa thambo; musamaiwala.