Woyamba ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake. Mowabu; yemweyo ndi atate wa Amowabu kufikira lero.
1 Samueli 14:47 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Saulo atakhazikitsa ufumu wa pa Israele, iye anaponyana ndi adani ake onse pozungulira ponse, ndi Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi Edomu ndi mafumu a Zoba, ndi Afilisti; ndipo paliponse anapotolokerapo, anawalanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Saulo atakhazikitsa ufumu wa pa Israele, iye anaponyana ndi adani ake onse pozungulira ponse, ndi Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi Edomu ndi mafumu a Zoba, ndi Afilisti; ndipo paliponse anapotolokerapo, anawalanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Saulo adakhala mfumu yolamulira Aisraele, adamenyana nkhondo ndi adani ake onse omzungulira. Adamenyana ndi Amowabu, Aamoni, Aedomu, mafumu a ku Zoba ndiponso Afilisti. Kulikonse kumene ankapita, ankaŵagonjetsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli ali mtsogoleri wa Israeli, anachita nkhondo ndi adani awa omuzungulira: Mowabu, Amoni, Edomu mafumu a ku Zoba ndi Afilisti. Kulikonse kumene ankapita ankawagonjetsa. |
Woyamba ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake. Mowabu; yemweyo ndi atate wa Amowabu kufikira lero.
Wamng'ono ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake Benami; yemweyo ndi atate wa Aamoni kufikira lero.
Uta wa Yonatani sunabwerere, ndipo lupanga la Saulo silinabwerere chabe, pa mwazi wa ophedwa, pa mafuta a amphamvuwo.
Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Beterehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu chikwi chimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri.
Ndipo Davide anakhala mfumu ya Aisraele onse, Davide naweruza ndi chilungamo milandu ya anthu onse.
Davide anakanthanso Hadadezere, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pomuka iye kukadzitengeranso ufumu wake ku chimtsinje cha Yufurate.
Ndipo Mulungu anamuutsira mdani wina, ndiye Rezoni mwana wa Eliyada, amene adathawa mbuye wake Hadadezere mfumu ya ku Zoba.
Ndipo Yehova sadanene kuti adzafafaniza dzina la Israele pansi pa thambo; koma anawapulumutsa ndi dzanja la Yerobowamu mwana wa Yehowasi.
Ndipo tsopano, siyi mfumu idzayendabe pamaso panu; ndipo ine ndine wokalamba waimvi; ndipo, onani, ana anga aamuna ali nanu, ndipo ine ndinayendabe pamaso panu kuyambira ubwana wanga kufikira lero.
Saulo anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ufumu wake; nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri.
Ndipo Saulo analeka kuwapirikitsa Afilistiwo; ndi Afilistiwo anamuka ku malo a iwo okha.
Ndipo panali nkhondo yowawa ndi Afilisti masiku onse a Saulo; ndipo Saulo pakuona munthu wamphamvu, kapena ngwazi, anamtenga akhale naye.
Tsono munthu wina wa anyamata a Saulo anali komweko, tsiku lija, anachedwetsedwa pamaso pa Yehova; dzina lake ndiye Doegi wa ku Edomu, kapitao wa abusa a Saulo.