1 Samueli 14:30 - Buku Lopatulika Koposa kotani nanga, ngati anthu akadadya nakhuta zowawanya anazipeza za adani ao? Popeza tsopano palibe kuwapha kwakukulu kwa Afilisti. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koposa kotani nanga, ngati anthu akadadya nakhuta zowawanya anazipeza za adani ao? Popeza tsopano palibe kuwapha kwakukulu kwa Afilisti. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kukadakhala bwino kwambiri, anthu akadadya mwaufulu lero zofunkha zimene adazipeza kwa adani ao. Zidakatero bwenzi tsopano lino titapha Afilisti ambiri.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zikanakhala zabwino kwambiri anthuwa akanadya lero zofunkha za adani awo. Zikanatero tikanapha Afilisti ochuluka.” |
Ndipo Yonatani anati, Atate wanga wavuta dziko; onani m'maso mwanga mwayera, chifukwa ndinalawako pang'ono uchiwu.
Ndipo anakantha Afilisti tsiku lija kuyambira ku Mikimasi kufikira ku Ayaloni, ndipo anthu anafooka kwambiri.