Nati iye, Sindimavute Israele ine ai, koma inu ndi nyumba ya atate wanu; popeza munasiya malamulo a Yehova, ndi kutsata Abaala.
1 Samueli 14:29 - Buku Lopatulika Ndipo Yonatani anati, Atate wanga wavuta dziko; onani m'maso mwanga mwayera, chifukwa ndinalawako pang'ono uchiwu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yonatani anati, Atate wanga wavuta dziko; onani m'maso mwanga mwayera, chifukwa ndinalawako pang'ono uchiwu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yonatani adati, “Bambo wanga wavutitsa anthu onse. Taonani ine m'maso mwanga mwayera, chifukwa ndalaŵako uchiwu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yonatani anati, “Abambo anga achita chinthu choyipira dziko. Taonani mʼmaso mwanga mwayera chifukwa ndalawa uchiwu pangʼono. |
Nati iye, Sindimavute Israele ine ai, koma inu ndi nyumba ya atate wanu; popeza munasiya malamulo a Yehova, ndi kutsata Abaala.
Penyani, ndiyankheni, Yehova Mulungu wanga. Penyetsani maso anga, kuti ndingagone tulo ta imfa;
Ndipo Yoswa anati, Watisautsiranji? Yehova adzakusautsa lero lino. Ndipo Aisraele onse anamponya miyala, nawatentha ndi moto, nawaponya miyala.
Ndipo wina wa anthuwo anayankha, nati, Atate wanu analangiza anthu kolimba ndi lumbiro, ndi kuti, Wotembereredwa iye wakudya lero chakudya. Ndipo anthuwo analema.
Koposa kotani nanga, ngati anthu akadadya nakhuta zowawanya anazipeza za adani ao? Popeza tsopano palibe kuwapha kwakukulu kwa Afilisti.