1 Samueli 14:27 - Buku Lopatulika Koma Yonatani sanamve m'mene atate wake analumbirira anthu; chifukwa chake iye anatambalitsa ndodo ya m'dzanja lake, naitosa m'chisa cha uchi, naika dzanja lake pakamwa pake; ndipo m'maso mwake munayera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yonatani sanamve m'mene atate wake analumbirira anthu; chifukwa chake iye anatambalitsa ndodo ya m'dzanja lake, naitosa m'chisa cha uchi, naika dzanja lake pakamwa pake; ndipo m'maso mwake munayera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Yonatani anali asanamve za temberero la bambo wake lija. Choncho adatosa chisa cha njuchi ndi nsonga ya ndodo imene inali m'manja mwake, naika uchi wake pakamwa naadya. Atatero m'maso mwake mudachita kuti ngwee. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Yonatani sanamve kuti abambo ake anawalumbirira anthu aja choncho anatenga ndodo yake imene inali mʼdzanja lake ndipo anayipisa mu chisa cha njuchi. Choncho iye anadya uchiwo ndipo mʼmaso mwake munayera. |
Monga kasupe wopondedwa, ndi chitsime choonongeka, momwemo wolungama ngati agonjera woipa.
Ndipo wina wa anthuwo anayankha, nati, Atate wanu analangiza anthu kolimba ndi lumbiro, ndi kuti, Wotembereredwa iye wakudya lero chakudya. Ndipo anthuwo analema.
Ndipo Yonatani anati, Atate wanga wavuta dziko; onani m'maso mwanga mwayera, chifukwa ndinalawako pang'ono uchiwu.
Pamenepo Saulo ananena ndi Yonatani, Undiuze chimene unachita. Ndipo Yonatani anamuuza, nati, Zoonadi ndinangolawako uchi pang'ono ndi nsonga ya ndodo inali m'dzanja langa: ndipo onani ndiyenera kufa.
nampatsanso chigamphu cha nchinchi ya nkhuyu ndi nchinchi ziwiri za mphesa; ndipo atadya, moyo wake unabweranso mwa iye; pakuti adagona masiku atatu ndi usiku wao, osadya chakudya, osamwa madzi.