1 Samueli 14:26 - Buku Lopatulika Ndipo pakufika anthuwo m'nkhalangomo, onani, madzi a uchi anachuluka; koma panalibe munthu mmodzi anaika dzanja lake pakamwa, pakuti anthuwo anaopa tembererolo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakufika anthuwo m'nkhalangomo, onani, madzi a uchi anachuluka; koma panalibe munthu mmodzi anaika dzanja lake pakamwa, pakuti anthuwo anaopa tembererolo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ataloŵa m'nkhalangomo, adangoona uchi ukukha pansi, koma panalibe amene adatengako kuika pakamwa, poti ankaopa temberero lija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atalowa mʼnkhalango, anaona uchi ukukha, koma palibe amene anadya, pakuti ankaopa lumbiro lija. |
Zonse zigwera onse chimodzimodzi; kanthu kamodzi kangogwera wolungama ndi woipa; ngakhale wabwino ndi woyera ndi wodetsedwa; ngakhale wopereka nsembe ndi wosapereka konse; wabwino alingana ndi wochimwa; wolumbira ndi woopa lumbira.
Ndipo Yohane yekhayo anali nacho chovala chake cha ubweya wangamira, ndi lamba lachikopa m'chuuno mwake; ndi chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wakuthengo.