ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.
Ndipo anaufula ndi dzanja lake, nayenda, namadya alimkuyenda, nadza kwa atate wake ndi amai wake, nawapatsa, nadya iwo; koma sanawauze kuti adaufula uchiwo m'chitanda cha mkango.