1 Samueli 14:24 - Buku Lopatulika Ndipo Aisraele anasauka tsiku lija; pakuti Saulo anawalumbirira, kuti, Atembereredwe iye wakudya kanthu kufikira madzulo, ndikabwezere chilango adani anga. Motero anthu onse anakhala opanda kudya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Aisraele anasauka tsiku lija; pakuti Saulo anawalumbirira, kuti, Atembereredwe iye wakudya kanthu kufikira madzulo, ndikabwezere chilango adani anga. Motero anthu onse anakhala opanda kudya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ankhondo a Aisraele adavutika tsiku limene lija, pakuti Saulo adaŵaopseza pakunena kuti, “Atembereredwe amene adye kanthu kusanade, ndisanalipsire adani anga.” Motero panalibe ndi mmodzi yemwe amene adalaŵa chakudya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma asilikali a Israeli anavutika tsiku limenelo, chifukwa Sauli anawalumbirira Aisraeli kuti, “Wotembereredwa munthu aliyense amene adzadya kusanade, ine ndisanalipsire adani anga!” Kotero palibe wankhondo aliyense amene analawa chakudya. |
Wonyoza Mulungu aononga mnzake ndi m'kamwa mwake; koma olungama adzapulumuka pakudziwa.
kapena munthu akalumbira ndi milomo yake osalingirira kuchita choipa, kapena kuchita chabwino, chilichonse munthu akalumbira osalingirira, ndipo chidambisikira; koma pochizindikira akhala wopalamula chimodzi cha izi:
Ndipo Israele analonjeza chowinda kwa Yehova, nati, Mukadzaperekatu anthu awa m'dzanja langa, ndidzaononga mizinda yao konse.
pamenepo wansembe alumbiritse mkazi lumbiro lakutemberera, ndi wansembe anene kwa mkazi, Yehova akuike ukhale temberero ndi lumbiro pakati pa anthu a mtundu wako, pakuondetsa Yehova m'chuuno mwako, ndi kukutupitsa thupi lako;
Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso.
Ndipo Yoswa anawalumbirira nyengo ija, ndi kuti, Wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzauka ndi kumanga mzinda uwu wa Yeriko; adzamanga maziko ake ndi kutayapo mwana wake woyamba, nadzaimika zitseko zake ndi kutayapo mwana wake wotsirizira.
Lemekezani Yehova pakuti atsogoleri mu Israele anatsogolera, pakuti anthu anadzipereka mwaufulu.
Pakuti, pali Yehova wakupulumutsa Israele, chingakhale chili m'mwana wanga Yonatani, koma adzafa ndithu. Koma pakati pa anthu onse panalibe mmodzi wakumyankha iye.
Nati Saulo, Mudzatero kwa Davide, kuti mfumu safuna cholowolera china, koma nsonga za makungu zana limodzi za Afilisti, kuti abwezere chilango adani a mfumu. Koma Saulo anaganizira kupha Davide ndi dzanja la Afilisti.