Pamenepo anthu a Israele analalikidwa kuchokera ku Nafutali, ndi ku Asere, ndi ku Manase yense, nalondola Amidiyani.
1 Samueli 14:22 - Buku Lopatulika Anateronso Aisraele onse akubisala m'phiri la Efuremu, pakumva kuti Afilisti anathawa, iwo anawapirikitsa kolimba kunkhondoko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anateronso Aisraele onse akubisala m'phiri la Efuremu, pakumva kuti Afilisti anathawa, iwo anawapirikitsa kolimba kunkhondoko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chimodzimodzinso Aisraele amene adaabisala m'dziko lamapiri la Efuremu, atamva kuti Afilisti akuthaŵa, nawonso adaŵathamangira Afilistiwo naŵathira nkhondo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngakhale Aisraeli amene ankabisala ku dziko lamapiri la Efereimu atamva kuti Afilisti akuthawa, nawonso anawathamangitsa Afilistiwo nawathira nkhondo. |
Pamenepo anthu a Israele analalikidwa kuchokera ku Nafutali, ndi ku Asere, ndi ku Manase yense, nalondola Amidiyani.
Pamene anthu a Israele anazindikira kuti ali m'kupsinjika, pakuti anthuwo anasauka mtima, anthuwo anabisala m'mapanga, ndi m'nkhalango, ndi m'matanthwe, ndi m'malinga, ndi m'maenje.
Ndipo onse awiri anadziwulula kwa a ku kaboma ka Afilistiwo; ndipo Afilistiwo anati, Onani, Ahebri alikutuluka m'mauna m'mene anabisala.
Ndipo pamene Aisraele akukhala tsidya lina la chigwa, ndi iwo akukhala tsidya la Yordani, anaona kuti Aisraele alikuthawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake anafa, iwowa anasiya mizinda yao, nathawa; ndipo Afilisti anadza nakhala m'menemo.