Pamenepo anthu a Israele analalikidwa kuchokera ku Nafutali, ndi ku Asere, ndi ku Manase yense, nalondola Amidiyani.
1 Samueli 14:21 - Buku Lopatulika Ndiponso Ahebri akukhala nao Afilisti kale, amene anatuluka m'dziko lozungulira kukalowa nao kuzithando; iwonso anatembenukira kuti akakhale ndi Aisraele amene anali ndi Saulo ndi Yonatani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiponso Ahebri akukhala nao Afilisti kale, amene anatuluka m'dziko lozungulira kukalowa nao kuzithando; iwonso anatembenukira kuti akakhale ndi Aisraele amene anali ndi Saulo ndi Yonatani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ahebri ena amene kale adaali pamodzi ndi Afilistiwo, ndipo anali atapita nao ku zithandozo, iwonso adatembenuka nakhala pamodzi ndi Aisraele a mbali ya Saulo ndi Yonatani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aheberi ena amene kale anali ndi Afilisti mpaka kukakhala ku misasa yawo, iwonso anatembenuka nakhala pamodzi ndi Aisraeli amene ankatsata Sauli ndi Yonatani. |
Pamenepo anthu a Israele analalikidwa kuchokera ku Nafutali, ndi ku Asere, ndi ku Manase yense, nalondola Amidiyani.
Koma akalonga a Afilisti anapsa naye mtima; nanena naye akalonga a Afilisti, Bwezani munthuyu, abwerere kumalo kwake kumene munamuikako, asatsikire nafe kunkhondo, kuti kunkhondoko angasanduke mdani wathu; pakuti uyu adzadziyanjanitsa ninji ndi mfumu yake? Si ndi mitu ya anthu awa?
Limbikani, ndipo muchite chamuna, Afilisti inu, kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga iwowa anali akapolo anu. Chitani chamuna nimuponyane nao.