Ndipo kunali tsiku lina kuti Yonatani mwana wa Saulo ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite kunka ku kaboma ka Afilisti, tsidya lija. Koma sanauze atate wake.
1 Samueli 14:2 - Buku Lopatulika Ndipo Saulo analikukhala m'matsekerezo a Gibea patsinde pa mtengo wankhangaza uli ku Migironi; ndipo panali naye anthu monga mazana asanu ndi limodzi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Saulo analikukhala m'matsekerezo a Gibea patsinde pa mtengo wankhangaza uli ku Migironi; ndipo panali naye anthu monga mazana asanu ndi limodzi; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Saulo ankakhala m'malire a Gibea patsinde pa mtengo wa makangaza ku Migironi. Anthu amene anali naye analipo 600 pamodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli ankakhala mʼmalire a Gibeya pa tsinde pa mtengo wamakangadza ku Migironi. Anthu amene anali naye analipo 600. |
Ndipo kunali tsiku lina kuti Yonatani mwana wa Saulo ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite kunka ku kaboma ka Afilisti, tsidya lija. Koma sanauze atate wake.
Pakumva Saulo kuti anadziwika Davide, ndi anthu ake akukhala naye, Saulo analikukhala mu Gibea, patsinde pa mtengo wa bwemba, m'dzanja lake munali mkondo wake, ndi anyamata ake onse anaimirira pali iye.