Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye.
1 Samueli 14:17 - Buku Lopatulika Pamenepo Saulo ananena ndi anthu amene anali naye, Awerenge tsopano, kuti tizindikire anatichokera ndani. Ndipo pamene anawerenga, onani Yonatani ndi wonyamula zida zake panalibe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Saulo ananena ndi anthu amene anali naye, Awerenge tsopano, kuti tizindikire anatichokera ndani. Ndipo pamene anawerenga, onani Yonatani ndi wonyamula zida zake panalibe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Saulo adauza anthu amene anali naye aja kuti, “Ŵerengani anthu, ndipo muwone amene achokapo.” Ataŵaŵerenga, adaona kuti Yonatani ndi mnyamata womnyamulira zida uja palibe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Sauli anawawuza anthu amene anali naye kuti, “Awerengeni asilikali kuti muona amene wachoka.” Atawawerenga anapeza kuti Yonatani ndi mnyamata wake womunyamulira zida zake za nkhondo palibe. |
Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye.
Ndipo ozonda a Saulo ku Gibea wa ku Benjamini anayang'ana; ndipo, onani, khamu la anthu linamwazikana, kulowa kwina ndi kwina.
Ndipo Saulo ananena ndi Ahiya, Bwera nalo likasa la Mulungu kuno. Pakuti likasa la Mulungu linali kumeneko masiku aja ndi ana a Israele.