Ndipo kudzachitika m'dziko lonse, ati Yehova, magawo awiri m'menemo adzalikhidwa nadzafa; koma gawo lachitatu lidzasiyidwa m'mwemo.
1 Samueli 13:21 - Buku Lopatulika ndipo mtengo wakukonza makasu, ndi zikhasu ndi makasu a mano unali masekeli awiri mwa atatu ndi mtengo wa nkhwangwazo; ndi kusongola zotwikira unali sekeli imodzi mwa atatu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo mtengo wakukonza makasu, ndi zikhasu ndi makasu a mano unali masekeli awiri mwa atatu ndi mtengo wa nkhwangwazo; ndi kusongola zotwikira unali sekeli imodzi mwa atatu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtengo wonoletsera nkhwangwa unali ndalama imodzi, ndipo mtengo wosanjitsira makasu ndi wosongoletsera zisonga unali ndalama ziŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtengo wonolera mapulawo ndi makasu unali zigawo ziwiri za sekeli, mtengo wonolera zisonga ndi nkhwangwa unali gawo limodzi la Sekeli. |
Ndipo kudzachitika m'dziko lonse, ati Yehova, magawo awiri m'menemo adzalikhidwa nadzafa; koma gawo lachitatu lidzasiyidwa m'mwemo.
koma Aisraele onse ankatsikira kwa Afilisti, kuti awasanjire munthu yense chikhasu chake, cholimira chake, nkhwangwa yake, ndi chisenga chake;
Chomwecho kunali kuti tsiku lankhondolo sunapezeke mkondo kapena lupanga m'manja a anthu onse anali ndi Saulo ndi Yonatani; koma Saulo yekha ndi Yonatani mwana wake anali nazo.