Pamenepo Saulo anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israele; zikwi za iwowa zinali ndi Saulo ku Mikimasi, ndi kuphiri la ku Betele; ndi chikwi chimodzi anali ndi Yonatani ku Gibea wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.
1 Samueli 13:15 - Buku Lopatulika Ndipo Samuele anauka nachoka ku Giligala kunka ku Gibea wa ku Benjamini. Ndipo Saulo anawerenga anthu amene anali naye, monga mazana asanu ndi limodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Samuele anauka nachoka ku Giligala kunka ku Gibea wa ku Benjamini. Ndipo Saulo anawerenga anthu amene anali naye, monga mazana asanu ndi limodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atatero Samuele adanyamuka ku Giligala napita ku Gibea ku dziko la Benjamini. Saulo adaŵerenga anthu amene anali naye, ndipo adapeza kuti alipo 600. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Samueli anachoka ku Giligala ndi kupita ku Gibeyati ku dziko la Benjamini. Saulo anawerenga anthu amene anali naye ndipo analipo 600. |
Pamenepo Saulo anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israele; zikwi za iwowa zinali ndi Saulo ku Mikimasi, ndi kuphiri la ku Betele; ndi chikwi chimodzi anali ndi Yonatani ku Gibea wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.
Ndipo Saulo analikukhala m'matsekerezo a Gibea patsinde pa mtengo wankhangaza uli ku Migironi; ndipo panali naye anthu monga mazana asanu ndi limodzi;
Ndipo Samuele analawirira m'mawa kuti akakomane ndi Saulo; ndipo munthu anamuuza Samuele kuti, Saulo anafika ku Karimele, ndipo taonani, anaimika chikumbutso chake, nazungulira, napitirira, natsikira ku Giligala.