1 Samueli 12:10 - Buku Lopatulika Ndipo anapemphera kwa Yehova, kuti, Tinachimwa, popeza tinasiya Yehova, ndi kutumikira Abaala ndi Asitaroti, koma mutipulumutse tsopano m'manja a adani anthu, ndipo tidzakutumikirani Inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapemphera kwa Yehova, kuti, Tinachimwa, popeza tinasiya Yehova, ndi kutumikira Abaala ndi Asitaroti, koma mutipulumutse tsopano m'manja a adani anthu, ndipo tidzakutumikirani Inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono iwowo adadandaula kwa Chauta nati. ‘Ife tachimwa chifukwa choti tasiya Inu Chauta, ndipo tatumikira mafano aja a Baala ndi Asitaroti. Koma tsopano tipulumutseni kwa adani athu, ndipo tidzakutumikirani.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono iwo analira kwa Yehova nati, ‘Ife tachimwa, chifukwa tamusiya Yehova ndi kumatumikira mafano a Baala ndi Asiteroti. Koma tsopano tilanditseni mʼmanja mwa adani athu ndipo tidzakutumikirani.’ |
Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.
ndi Giliyadi logawika pakati, ndi Asitaroti ndi Ederei, mizinda ya ufumu wa Ogi mu Basani, inali ya ana a Makiri mwana wa Manase, ndiwo ana a Makiri ogawika pakati, monga mwa mabanja ao.
Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova ndi kuti, Takuchimwirani, popeza tasiya Mulungu wathu ndi kutumikira Abaala.
Koma pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova, Yehova anawaukitsira mpulumutsi, Ehudi mwana wa Gera, Mbenjamini, munthu wamanzere, ndipo ana a Israele anatumiza mtulo m'dzanja lake kwa Egiloni mfumu ya Mowabu.
Ndipo ana a Israele anachita choipa pamaso pa Yehova, naiwala Yehova Mulungu wao, natumikira Abaala ndi zifanizo.
Ndipo pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova, Yehova anaukitsira ana a Israele mpulumutsi amene anawapulumutsa, ndiye Otiniyele mwana wa Kenazi, mng'ono wake wa Kalebe.
Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova; pakuti anali nao magaleta achitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israele kolimba zaka makumi awiri.
Ndipo kunali, kuti likasalo linakhala nthawi yaikulu mu Kiriyati-Yearimu; popeza linakhalako zaka makumi awiri; ndipo banja lonse la Israele linalirira Yehova.
Ndipo anaunjikana ku Mizipa, natunga madzi, nawatsanula pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lija, nati, Tinachimwira Yehova. Ndipo Samuele anaweruza ana a Israele mu Mizipa.